kusowa zochita mmudzimu,
maka tikaweluka kuminda,
timangoti khale khale mmakonde,
ngati nkhuku zowutila,
popanda zisangalalo kuli chuu
kudikilaso kuche tikaswe mphanje
ndiye poti awa amabweletsa magule,
tonse timangoti unji unji komweko
tikatakasuke kutopesa pakhomo.
kuno timabwelera magule,
pokhapo ndiye ndiwulule,
osati nthano zawozo za mthira,
tinatopa ndi kumatidwa phula,
ndi awa otidyela masuku pa mutu,
muwaona akafika pa mpando,
safuna kuponda mudzi wawo,
ati tiwalodza ndife a thakati,
ife amene tidawasankha,
atatiudza atibweletsela chitutuko.
Lero akana kumwa madzi athu,
akuti awacheka mmimba.
Ife timwa zithaphwi zomwezo,
iwo amwa a mmabotolo ogula.
Ana awo aphunzira ndi azungu,
ife athu aphunzilira pa mtengo.
Apita ku zipatala za pamwamba,
ife ichi chipatala chisowa azamba.
Akhala mwa ngwee mmagetsi,
Ife tingolowa mu mdima wogwilika.
No comments:
Post a Comment