Saturday, 21 July 2012

KAYA AMAGANIZA BWANJI ANTHUWA

KAYA AMAGANIZA BWANJI ANTHUWA.

Anzathu ali pataliwo amakhalitsa,
koma ife aliyense atinyanyamila.
Ndi awo omwe owopa utali,
amantha kukwela mmwambawo,
nawonso apezelapo mphumi,
ena angotitengela lung'wanu.
Kaya amaganiza bwanji anthuwa.
Kusilira anzathu akamasintha,
akamacha kuvala za chikasu.

Ife timangothela biliwili,
sitifika patali amangotipulula.
Ena amakatiundika mmanguti,
koma si tonse timalama.
Kaya amaganiza bwanji anthuwa.
Ena atichotsa mchimake,
ndiye timayambapo kunyala,
kenako kusanduka zinyalala,
Ena ndiye atiyesa ngati miyala,
yolasila awo ali patali.
ativunga, tiphulika,tigwa chikaa!
Kaya amaganiza bwanji anthuwa.
Koma manthuyu amayesetsa zedi.
kuwapatsa mphepo ya yezi yezi,
kuwapatsa chakudya, mthunzi,
kuwasungila madzi mu nthaka,
kuwakongoletsela dzikoli,
koma iwo atitseketa tonse
Kaya amaganiza bwanji anthuwa.

No comments:

Post a Comment