Saturday 4 May 2013

PATSOGOLO

Mwina timavutika pa Nyanja ya msautso,
ndi namondwe akuomba amalondola dzuwa,
koma mdziko la ngwiro, zitachoka nkhunguzo!
tidzazindikila bwino pa tsogolo

chorus.
pa tsogolo mmene mawu abwera,
pamene woyera adzafika kwawo,
tidzanena nthano tagonjetsa bwanji?
tidzazindikila bwino patsogolo.

Zofunika zathuzi nzosoweka mdzikoli,
mthupi, njala ndi usiwa, mminda milibe mmela,
tikhulupile mbuye ndi malinga ndi mawu,
tidzazindikila bwino patsogolo
(bwelezani kolasi)

mbali zonse zovuta zosazindikilika,
njira zosiyana zofika ku dziko la lonjezo,
Mulungu azatisunga mpaka tsiku la imfa,
tidzazindikila bwino pa tsogolo
(bwelezani kolasi)

Ife mwina tigwidwa ndi nsapha wobisika,
mtima upweteka tikanena mawu wolakwa,
tikafunsa chifukwa chomwe timayesedwa,
tidzazindikila bwino patsogolo
(bwelezani kolasi)