Tadza kudzailambila ili kuti?
mfumu yathu, mfumu ya mafumu.
Uthenga wochoka kwa anzeru aku m'mawa,
Uthenga wopatsa phuma kwa mfumu Herold,
Khanda labadwali si khanda wamba ayi.
Anthunthumila mfumu Herold,
mphamvu zili mwa mwana wabadwa ku Bethlehem,
zaposa mphamvu izo zili mu ufumu wake.
Asowa tulo pogona pake,
khanda labadwali si khanda wamba ayi.
Asowa mtendere a mfumu Herold,
alingilira kuchita choipitsitsa,
afunitsitsa kupha makanda onse ndithu,
khanda labadwa ku Bethlehem si khanda wamba,
ndi mfumu yopatsa moyo,
mfumu ya mtendere,
mfumu ya mafumu,
mfumu ya chilungamo.
No comments:
Post a Comment