Tamvelani a chimwene a Madigadi,
Kaya ulendo munayenda bwanji wa ku tawuni? ife kuno tinasala bwino, ndiyesa nchito munaipeza.
Kuno mng'ono wanu KALIYALA anakhonza mayeso kupita ku sekondale ndiye timapempha ndalama za ku sukuluko.
Timatinso SIPINDULO abwele azakhale nanu ku tawuniko azaphunzile sukulu za komweko.
Mulongo wanu akusowa yunifolomu ya ku sukulu.
Amai anu akusowa ndalama ya ku chipatala anatuluka katulutulu akuvutika kwambiri ndi mwendo.
Minda tinamaliza kulima koma timapempha ndalama ya feteleza, chaka chinonso mwayi wa makuponi watipita.Ngatinso kumeneko kukupezeka makasu mutigulireko.
Khoma limodzi la nyumba linagwa timapempha ndalama zoti tikonzele.
Achimwene anu a SIPOKOLO amapempha ndalama yoti ayambile geni.
Pomaliza mutangochoka panafika milandu yochoka kwa a THEYALA akuti munapasa pathupi mtsikana wawo, mtsikanayo abwela komweko azamutule ndi amalume ake a HANDULO.
Ndatha ine bambo wanu.
Chinanso ndimati ngati munganditumizile ndalama zoti ndibweze ngongole kwa a CHUBU tinatenga ka ndiwo anaphako ka mbuzi.
Zikomo
Ine bambo wanu
che Basikolo.
No comments:
Post a Comment