Tuesday, 18 March 2014

INE ANGA NDI OMWEWA A NACHISALE

Ine anga ndi omwewa a Nachisale,
lero akundipatsa la pa thumba,
kudyetsa yonse iyi mbumba,
poti ine ndili khwakhwa khwaa!
ngakhale lobowola ndilibe,
wandikhudzumutsa ulova,
abale anzanga ndinkangomva.
lero ndasanduka zungulira khonde,
chasosola mapiko chiomba nkhanga
Ine ndi khobidi tinali mabwenzi,
timakumana mwezi ndi mwezi,
ndiye ndimati ndikayela mmanja,
ndimatsakamila pa Njira ili Kuti,
kumwelera ndi kukhwasula,
osalephelanso a nkupa nkupa,
akupe ngumbi zotengeka ndi kuwala,
zoti tili ndi ana kuiwala.
ndani achisiya chinyamata ichi.
ndikakumbuka mnsana wa njira,
ndimagula mpiru wa a biti Machenje,
a Nachi ndi ana akadye kunyumba,
ine nditatsuka kale mkamwa,
lero mchokochi unafikila ine,
a Nachi ndi amene akutidyetsa,
palibenso zotsuka mkamwa mobisa
bola iwo abweletsa timatemba
palibe icho apanga mozemba.
Ine anga ndi omwewa a Nachisale,
ndaona mmene avutikila ndi anawa,
osati aja odzola zonga dothi,
osamva ndi ifeyo a gonthi,
timangolonda tili pulipuli,
atikolole akasokelele dzala.
ndikapeza ina ntchito,
ndidzapita ku nyanja ndi a Nachisale
ndi anawa tikasangalale.

No comments:

Post a Comment