Nyimbo izi zitsefukila mu mtima mwanga,
sizichoka pa kamwa panga,
zituluka ngati katsupe,
mukandizodza ine Yehova!
nditsila mnsembe iyi nthawi zonse
sinditopa kuimba nyimbo za matamando,
ngati ka mbalame ako ka munkhalango.
Mtima wanga umveka yazi yazi
nyimbo za ukulu wanu zitsitsa mtima
zindipatsa chimwemwe
kafungo kabwino ka kuzodza
kandifikila inenso
kafikila kwa inu mfumu
kaposa mnsembe yopseleza.
No comments:
Post a Comment